Isaiah 29:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsoka kwa amene amabisira Chauta maganizo ao, amene amachita ntchito zao mu mdima, namaganiza kuti palibe amene akuŵaona ndi kudziŵa zimene akuchita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsoka kwa iwo amene afunitsa kubisira Yehova uphungu wao, ndi ntchito zao zili mumdima, ndipo amati ndani ationa ife? Ndani atidziwa ife?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsoka kwa amene amayesetsa kubisira Yehova maganizo awo, amene amachita ntchito zawo mu mdima nʼkumanena kuti, “Ndani amene akundiona kapena ndani akudziwa zimene ndikuchita?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsoka kwa iwo amene afunitsa kubisira Yehova uphungu wao, ndi nchito zao ziri mumdima, ndipo amati Ndani ationa ife? ndani atidziwa ife?