Isaiah 29:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwazondotsa zinthu zonse. Kodi chopambana nchiti, woumba kapena dothi loumbira? Kodi chinthu chopangidwa chingauze wochipanga kuti, “Sudandipange ndiwe?” Monga chingamuuze kuti, “Sukudziŵa chimene ukuchita?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ozolitsa inu! Kodi woumba adzayesedwa ngati dothi; kodi chinthu chopangidwa chinganene za iye amene anachipanga, Iye sanandipange ine konse; kapena kodi chinthu choumbidwa chinganene za iye amene anachiumba, Iye alibe nzeru?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu mumazondotsa zinthu ngati kuti dothi lasanduka wowumba mbiya. Kodi chinthu chopangidwa chingawuze wochipanga kuti “Sunandipange ndi iwe?” Kapena mʼphika kunena kwa amene anawuwumba kuti, “Iwe sudziwa chilichonse?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ozolitsa inu! Kodi woumba adzayesedwa ngati dothi; kodi cinthu copangidwa cinganene za iye amene anacipanga, Iye sanandipanga ine konse; kapena kodi cinthu coumbidwa cinganene za iye amene anaciumba, Iye alibe nzeru?