Isaiah 29:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu adzalanga anthu osinjirira anzao, ndiponso ophophonyetsa anthu ozengedwa mlandu. Adzalanganso amene amapereka umboni wonama, kuti anzao osalakwa asaweruzidwe molungama.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
amene apalamulitsa munthu mlandu, namtchera msampha iye amene adzudzula pachipata, nambweza wolungama ndi chinthu chachabe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova adzalanga amene amasinjirira munthu kuti apezeke wolakwa, kapena kuphophonyetsa anthu ozenga mlandu ndi umboni wonama kuti osalakwa asaweruzidwe mwachilungamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
amene apalamulitsa munthu mlandu, namchera msampha iye amene adzudzula pacipata, nambweza wolungama ndi cinthu cacabe.