Isaiah 29:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero tsono Chauta, Mulungu wa Israele, amene adapulumutsa Abrahamu pa mavuto, akunena kuti, “Anthu anga sadzanyozedwanso, nkhope zao sizidzagwanso ndi manyazi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake Yehova amene anaombola Abrahamu, atero za banja la Yakobo: Yakobo sadzakhala ndi manyazi tsopano, ngakhale nkhope yake tsopano sidzagwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Yehova amene anawombola Abrahamu, akunena kwa zidzukulu za Yakobo kuti, “Anthu anga sadzachitanso manyazi; nkhope zawo sizidzagwanso ndi manyazi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace Yehova amene anaombola Abrahamu, atero za banja la Yakobo: Yakobo sadzakhala ndi manyazi tsopano, ngakhale nkhope yace tsopano sidzagwa.