Isaiah 29:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwo, ndiye kuti ana ao, akadzaona zimene ndidachita Ine pakati pao, adzatamanda dzina langa loyera. Adzazindikira kuyera kwake kwa Woyera Uja wa Yakobe, ndipo adzachita naye mantha Mulungu wa Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma pamene iye aona ana ake, ntchito ya manja anga, pakati pa iye, iwo adzayeretsa dzina langa; inde, iwo adzayeretsa Woyera wa Yakobo, nadzaopa Mulungu wa Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akadzaona ana awo ndi ntchito ya manja anga pakati pawo, adzatamanda dzina langa loyera; adzazindikira kuyera kwa Woyerayo wa Yakobo, ndipo adzachita naye mantha Mulungu wa Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma pamene iye aona ana ace, nchito ya manja anga, pakati pa iye, iwo adzayeretsa dzina langa; inde, iwo adzayeretsa Woyera wa Yakobo, nadzaopa Mulungu wa Israyeli.