Isaiah 29:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono iwe Yerusalemu utagwetsedwa, udzalankhula uli pansi, mau ako adzamveka uli m'fumbi. Liwu lako lidzafumira pansi ngati la mzukwa, mau ako adzamveka ngati onong'ona kuchokera m'fumbi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwe udzagwetsedwa pansi, nudzanena uli pansi, ndi kulankhula kwako kudzakhala pansi kotuluka m'fumbi; ndi mau ako adzakhala ngati a wina amene ali ndi mzimu wobwebweta, kuchokera pansi, ndi kulankhula kwako kudzakhala konong'ona kochokera m'fumbi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Utagwetsedwa pansi, iwe udzayankhula kuchokera mʼnthaka, mawu ako adzatuluka uli mʼfumbi, adzamveka ngati a mzukwa. Mawu ako adzamveka ngati onongʼona kuchokera mʼfumbi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwe udzagwetsedwa pansi, nudzanena uli pansi, ndi kulankhula kwako kudzakhala pansi koturuka m'pfumbi; ndi mau ako adzakhala ngati a wina amene ali ndi mzimu wobwebweta, kucokera pansi, ndi kulankhula kwako kudzakhala konong'ona kocokera m'pfumbi,