Isaiah 29:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwe Yerusalemu, chigulu cha adani ako chidzamwazika ngati fumbi, chigulu cha ankhondo ankhanza chidzabalalika ngati mungu wouluka. Ndipo mwadzidzidzi ndi mosayembekezeka,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma khamu la achilendo ako lidzafanana ndi fumbi losalala, ndi khamu la oopsa lidzakhala monga mungu wochokachoka; inde kudzaoneka modzidzimuka dzidzidzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma chigulu cha adani ako chidzasanduka chifwirimbwiti. Chigulu cha ankhondo achilendo chidzabalalika ngati mungu wowuluzika ndi mphepo. Mwadzidzidzi ndi mosayembekezereka,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma khamu la acilendo ako lidzafanana ndi pfumbi losalala, ndi khamu la oopsya lidzakhala monga mungu wocokacoka; inde kudzaoneka modzidzimuka dzidzidzi.