Isaiah 29:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono chigulu cha mitundu ina yonse ya anthu othira nkhondo mzinda wa Ariyele, onse olimbana ndi mzindawo ndiponso linga lake lamphamvu ndi kuuzinga, onsewo adzazimirira ngati maloto, ngati zinthu zoziwona m'masomphenya usiku.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo khamu la mitundu yonse yomenyana ndi Ariyele, ngakhale yonse yomenyana naye ndi linga lake, ndi kumsautsa idzafanana ndi loto, masomphenya a usiku.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono chigulu chankhondo cha mitundu ina yonse chimene chikulimbana ndi mzinda wa Arieli nʼkumathira nkhondo mzindawo, malinga ake ndi kuwuzinga, chigulu chonsecho chidzazimirira ngati maloto, gati zinthu zoziona mʼmasomphenya usiku.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo khamu la mitundu yonse yomenyana ndi Arieli, ngakhale yonse yomenyana naye ndi linga lace, ndi kumsautsa idzafanana ndi loto, masomphenya a usiku.