Isaiah 29:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chigulu cha mitundu ina yonse ya anthu othira nkhondo Phiri la Ziyoni chidzakhala ngati munthu wanjala wolota kuti alikudya, koma podzuka, ali nayobe njala, kapena chidzakhalanso ngati munthu waludzu wolota kuti alikumwa, koma podzuka, kum'mero kudakali gwaa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudzafanana ndi munthu wanjala, pamene alota, ndipo, taonani, akudya; koma auka, ndipo m'kati mwake muli zii; kapena monga munthu waludzu pamene alota, ndipo taonani, akumwa; koma auka ndipo taonani walefuka, ndipo m'kati mwake muli gwa; momwemo lidzakhala khamu la mitundu yonse yomenyana ndi phiri la Ziyoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chidzakhala ngati munthu wanjala wolota akudya, koma podzuka ali nayobe njala; kapena ngati munthu waludzu wolota akumwa, koma podzuka, ali nalobe ludzu, kummero kwake kuli gwaa. Izi zidzachitika pamene chigulu cha nkhondo cha mitundu ina yonse chikunthira nkhondo Phiri la Ziyoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudzafanana ndi munthu wanjala, pamene alota, ndipo, taonani, akudya; koma auka, ndipo m'kati mwace muli zi; kapena monga munthu waludzu pamene alota, ndipo, taonani, akumwa; koma auka ndipo taonani walefuka, ndipo m'kati mwace muli gwa; momwemo lidzakhala khamu la mitundu yonse yomenyana ndi phiri la Ziyoni.