Isaiah 3:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsopano Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, ali pafupi kulanda Yerusalemu ndi Yuda chithandizo cha mtundu uliwonse chimene anthu amadalira. Adzachotsa chakudya chonse, adzachotsa madzi onse,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo onani, Ambuye, Yehova wa makamu, wachotsa ku Yerusalemu ndi ku Yuda mchirikizo wochirikiza chakudya chonse ndi madzi onse, zimene zinali mchirikizo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Taonani tsopano, Ambuye Yehova Wamphamvuzonse, ali pafupi kuchotsa mu Yerusalemu ndi mu Yuda zinthu pamodzi ndi thandizo; adzachotsa chakudya chonse ndi madzi onse,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo onani, Ambuye, Yehova wa makamu, wacotsa ku Yerusalemu ndi ku Yuda mcirikizo wocirikiza cakudya conse ndi madzi onse, zimene zinali mcirikizo;