Isaiah 3:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akuŵaimba mlandu akuluakulu ndi atsogoleri a anthu ake. Akuŵazenga kuti, “Ndinu amene mwaononga munda wanga wamphesa. Nyumba zanu zadzaza ndi zinthu zolanda kwa amphaŵi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova adzalowa m'bwalo la milandu ndi okalamba a anthu ake, ndi akulu ake: Ndinu amene mwadya munda wamphesa, zofunkha za waumphawi zili m'nyumba zanu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akuwazenga milandu akuluakulu ndi atsogoleri a anthu ake: “Ndinu amene mwawononga munda wanga wa mpesa; nyumba zanu zadzaza ndi zolanda kwa amphawi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova adzalowa monenera mirandu ndi okalamba a anthu ace, ndi akuru ace: Ndinu amene mwadya munda wamphesa, zofunkha za waumphawi ziri m'nyumba zanu;