Isaiah 3:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adati, “Akazi a ku Ziyoni ngodzikuza kwambiri: amayenda makosi ali wee, amayang'ana ndi maso ophika. Amayenda nyang'anyang'a ndi kuliza zigwinjiri zam'miyendo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Komanso Yehova ati, Chifukwa kuti ana akazi a Ziyoni angodzikuza atakweza makosi ao, ndi maso ao adama nayenda nanyang'ama poyenda pao naliza zigwinjiri za mapazi ao;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akunena kuti, “Akazi a ku Ziyoni ngodzikuza kwambiri, akuyenda atakweza makosi awo, akukopa amuna ndi maso awo akuyenda monyangʼama akuliza zigwinjiri za mʼmiyendo yawo
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Komanso Yehova ati, Cifukwa kuti ana akazi a Ziyoni angodzikuza atakweza makosi ao, ndi maso ao adama nayenda nanyang'ama poyenda pao naliza zigwinjiri za mapazi ao;