Isaiah 3:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'malo mwa kununkhira padzakhala kununkha, m'malo mwa lamba adzavala chingwe, m'malo mwa tsitsi lopesa bwino adzakhala ndi mipala, m'malo mwa delesi la mtengo wapatali adzavala chiguduli, m'malo mwa kunyadira kukongola adzachita manyazi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo padzakhala m'malo mwa zonunkhiritsa mudzakhala zovunda; ndi m'malo mwa lamba chingwe; ndipo m'malo mwa tsitsi labwino dazi; m'malo mwa chovala chapachifuwa mpango wachiguduli; zipsera m'malo mwa ukoma.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼmalo mwa kununkhira azidzanunkha, mʼmalo mwa lamba, adzavala chingwe; mʼmalo mwa tsitsi lopesa bwino, adzakhala ndi dazi; mʼmalo mwa zovala zabwino, adzavala chiguduli; mʼmalo mwa kunyadira kukongola adzachita manyazi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo padzakhala m'malo mwa zotsekemera mudzakhala zobvunda; ndi m'malo mwa lamba cingwe; ndipo m'malo mwa tsitsi labwino dazi; m'malo mwa cobvala ca pacifuwa mpango waciguduli; zipsera m'malo mwa ukoma.