Isaiah 3:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku limenelo mbale wakeyo adzayankha kuti, “Ine ai toto! Mavuto otereŵa ndilibe mankhwala ake, m'nyumba mwanga momwe ndilibe chakudya kapena chovala. Musaike ine kuti ndikhale mtsogoleri wa anthu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
tsiku limenelo adzakweza mau ake, kuti, Sindine wochiritsa, chifukwa kuti m'nyumba mwanga mulibe chakudya kapena chovala; inu simudzandiyesa ine wolamulira anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma tsiku limenelo mʼbale wakeyo adzafuwula kuti, “Ayi, mavuto oterewa ndilibe mankhwala ake. Ndilibe chakudya kapena chovala mʼnyumba mwanga; musasankhe ine kukhala mtsogoleri wa anthu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
tsiku limenelo adzakweza mau ace, kuti, Sindine wociritsa, cifukwa kuti m'nyumba mwanga mulibe cakudya kapena cobvala; inu simudzandiyesa ine wolamulira anthu.