Isaiah 3:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zoonadi Yerusalemu akusakazika ndipo Yuda akugwa, chifukwa zokamba ndiponso ntchito za anthu am'menemo nzonyoza Chauta. Salabadako za ulemerero wa Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa kuti Yerusalemu wapasulidwa, ndi Yuda wagwa; chifukwa kuti lilime lao ndi machitidwe ao akana Yehova, kuti autse mkwiyo wa m'maso a ulemerero wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yerusalemu akudzandira, Yuda akugwa; zokamba zawo ndi ntchito zawo nʼzotsutsana ndi Yehova, sakulabadira ulemerero wa Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa kuti Yerusalemu wapasulidwa, ndi Yuda wagwa; cifukwa kuti lilume lao ndi macitidwe ao akana Yehova, kuti autse mkwiyo wa m'maso a ulemerero wace.