Isaiah 3:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Maonekedwe a nkhope zao amaŵatsutsa. Amachimwa poyera ngati m'mene ankachitira anthu a mu Sodomu, sabisa konse. Tsoka kwa iwowo, achita kudziputira okha mavuto.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Maonekedwe a nkhope zao awachitira iwo mboni; ndipo amaonetsa uchimo wao monga Sodomu, saubisa. Tsoka kwa moyo wao! Chifukwa iwo anadzichitira zoipa iwo okha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Maonekedwe a nkhope zawo amawatsutsa; amaonetsera poyera tchimo lawo ngati Sodomu; salibisa tchimo lawolo. Tsoka kwa iwo odziputira okha mavuto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Maonekedwe a nkhope zao awacitira iwo mboni; ndipo amaonetsa ucimo wao monga Sodomu, saubisa. Tsoka kwa moyo wao! cifukwa iwo anadzicitira zoipa iwo okha.