Isaiah 30:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akuti, “Tsoka kwa ana ondipandukira Ine! Amachita zodzikonzera okha osati zokonza Ine. Amachita chipangano chaochao, chosatsata chifuniro changa, ndipo amanka nachimwirachimwira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsoka kwa ana opanduka, ati Yehova, amene atenga uphungu koma si pa Ine; napangana pangano opanda mzimu wanga, kuti aonjezere tchimo ndi tchimo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akuti, “Tsoka kwa ana ondipandukira amene amachita zowakomera iwo okha osati Ine, nachita mgwirizano wawowawo koma osati motsogozedwa ndi Ine. Choncho amanka nachimwirachimwira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsoka okhulupirira Aigupto. Tsoka kwa ana opanduka, ati Yehova, amene atenga uphungu koma si pa Ine; napangana pangano opanda mzimu wanga, kuti aonjezere cimo ndi cimo;