Isaiah 30:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake tchimo lanuli lidzakhala ngati mng'ankha pa chipupa chachitali choŵinuka, chimene kugwa kwake nkwadzidzidzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa chake kuipa kumeneku kudzakhala kwa inu monga pogumuka pofuna kugwa, monga potukuka m'khoma lalitali, kugumuka kwake kufika modzidzimutsa dzidzidzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
choncho tchimo linalo lidzakhala ngati mingʼalu pa khoma lalitali ndi lopendama limene linagwa mwadzidzidzi ndi mwamsangamsanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa cace kuipa kumeneku kudzakhala kwa inu monga pogumuka pofuna kugwa, monga potukuka m'khoma lalitari, kugumuka kwace kufika modzidzimutsa dzidzidzi.