Isaiah 30:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Ambuye Chauta, Woyera uja wa Israele adati, “Ngati mutembenuka ndi kubwerera, mudzapulumuka. Ngati mudzinga ndi kukhulupirira, mudzakhala amphamvu.” Koma inu mudakana kutero.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti atero Ambuye, Yehova Woyera wa Israele, M'kubwera ndi m'kupuma inu mudzapulumutsidwa; m'kukhala chete ndi m'kukhulupirira mudzakhala mphamvu yanu; ndipo simunafuna.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zimene Ambuye Yehova, Woyerayo wa Israeli ananena ndi izi: “Ngati mubwerera ndi kupuma mudzapulumuka, ngati mukhala chete ndi kukhulupirira mudzakhala amphamvu, koma inu munakana zimenezi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti atero Ambuye, Yehova Woyera wa Israyeli, M'kubwera ndi m'kupuma inu mudzapulumutsidwa; m'kukhala cete ndi m'kukhulupirira mudzakhala mphamvu yanu; ndipo simunafuna.