Isaiah 30:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu chikwi chimodzi mwa inu adzathaŵa poona mdani mmodzi. Asilikali asanu okha adzakwanira kukuthamangitsani. Otsalira mwa inu adzakhala ngati mtengo wa mbendera wapaphiri, ngati chizindikiro chapagomo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chikwi chimodzi chidzathawa pakuwadzudzula mmodzi; pakukudzudzulani anthu asanu mudzathawa; kufikira inu mudzasiyidwa ngati mlongoti pamwamba pa phiri, ndi ngati mbendera pamwamba pa chitunda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu 1,000 mwa inu adzathawa poona mdani mmodzi; poona adani asanu okha nonsenu mudzathawa. Otsala anu adzakhala ngati mbendera pa phiri, ndi ngati chizindikiro cha pa chulu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cikwi cimodzi cidzathawa pakuwadzudzula mmodzi; pakukudzudzulani anthu asanu mudzathawa; kufikira inu mudzasiyidwa ngati mlongoti pamwamba pa phiri, ndi ngati mbendera pamwamba pa citundu.