Isaiah 30:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndithudi, inu anthu a ku Ziyoni, okhala ku Yerusalemu, simudzaliranso. Mulungu adzakukomerani mtima pamene adzamva kulira kwanu, ndipo akadzangomva, pompo adzakuyankhani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti anthu adzakhala m'Ziyoni pa Yerusalemu; iwe sudzaliranso, Iye ndithu adzakukomera mtima pakumveka kufuula kwako; pakumva Iye adzayankha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu anthu a ku Ziyoni, amene mukhala mu Yerusalemu simudzaliranso. Mulungu adzakukomerani mtima pamene adzamva kulira kwanu kopempha thandizo! Ndipo akadzamva, adzakuyankhani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti anthu adzakhala m'Ziyoni pa Yerusalemu; iwe sudzaliranso, Iye ndithu adzakukomera mtima pakumveka kupfuula kwako; pakumva Iye adzayankha.