Isaiah 30:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo mudzatenga mafano anu, ena okutidwa ndi siliva, ena okutidwa ndi golide, ndipo mudzaŵataya ngati zinyalala, ndikunena kuti, “Zichoke zonsezi!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mudzaipitsa chokuta cha mafano ako, osema asiliva, ndi chomata cha mafano ako osungunula agolide; udzawataya ngati kanthu konyansa, udzati kwa iwo, Chokani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo mudzawononga mafano anu okutidwa ndi siliva ndiponso zifanizo zanu zokutidwa ndi golide; mudzawataya ngati zinthu zonyansa ndipo mudzati, “Zichoke zonsezi!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mudzaipitsa cokuta ca mafano ako, osema asiliva, ndi comata ca mafano ako osungunula agolidi; udzawataya ngati kanthu konyansa, udzati kwa iwo, Cokani.