Isaiah 30:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa tsiku limene nsanja zankhondo za adani anu zidzagwe, anthu ake naphedwa, pa phiri lililonse lalikulu ndi pa gomo lililonse lalitali, padzayenda mitsinje ya madzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamwamba pa mapiri akulu onse, ndi pa zitunda zonse zazitalitali padzakhala mitsinje ndi micherenje ya madzi, tsiku lophana lalikulu, pamene nsanja zidzagwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa tsiku limene adani anu adzaphedwa ndi nsanja zawo kugwa, mitsinje ya madzi idzayenda pa phiri lililonse lalikulu ndi pa phiri lililonse lalingʼono.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamwamba pa mapiri akuru onse, ndipa zitunda zonse zazitaritari padzakhala mitsinje ndi micerenje ya madzi, tsiku lophana lalikuru, pamene nsanja zidzagwa.