Isaiah 30:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwezi udzaŵala ngati dzuŵa, ndipo dzuŵa lidzaŵala kwambiri ngati kasanunkaŵiri kuŵala kwa pa tsiku limodzi. Zimenezi zidzachitika pamene Chauta adzamange ndi kupoletsa zilonda zimene Iye yemwe adachititsa pakuŵalanga anthu ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Komanso kuwala kwake kwa mwezi kudzakhala ngati kuwala kwa dzuwa, ndi kuwala kwa dzuwa kudzakula monga madzuwa asanu ndi awiri, monga kuwala kwa masiku asanu ndi awiri, tsiku limenelo Yehova adzamanga bala la anthu ake, nadzapoletsa khana limene anawakantha ena.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwezi udzawala ngati dzuwa, ndipo kuwala kwa dzuwa kudzawonjezereka kasanu nʼkawiri, ngati kuwala kwa tsiku limodzi. Yehova adzamanga mabala a anthu ake ndi kupoletsa zilonda zimene Iye anachititsa polanga anthu ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Komanso kuwala kwace kwa mwezi kudzakhala ngati kuwala kwa dzuwa, ndi kuwala kwa dzuwa kudzakula monga madzuwa asanu ndi awiri, monga kuwala kwa masiku asanu ndi awiri, tsiku limenelo Yehova adzamanga bala la anthu ace, nadzapoletsa khana limene anawakantha ena.