Isaiah 30:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onani, ulemerero wa Chauta ukuwonekera kuchokera kutali. Akuwonetsa mkwiyo m'kati mwa moto ndi m'kati mwa chiwutsi chatolotolo. Akulankhula mwaukali, ndipo mau ake akutentha ngati moto woononga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, dzina la Yehova lichokera kutali, mkwiyo wake uyaka, malawi ake ndi akulu; milomo yake ili yodzala ndi ukali, ndi lilime lake lili ngati moto wonyambita;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Taonani, Yehova akubwera kuchokera kutali, ndipo mkwiyo wake ndiwonyeka ndi chiweruzo chake chidzakhala chopweteka. Iye wayankhula mwaukali kwambiri, ndipo mawu ake ali ngati moto wonyeka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, dzina la Yehova licokera kutari, mkwiyo wace uyaka, malawi ace ndi akuru; milomo yace iri yodzala ndi ukali, ndi lilime lace liri ngati moto wonyambita;