Isaiah 30:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mpweya wake uli ngati mtsinje wosefukira, wa madzi oyesa m'khosi. Akusefa anthu a mitundu ina ndi sefa wosakaza. Ngati akavalo, akuŵaika m'kamwa chitsulo choti chiŵasokeretse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi mpweya wake uli ngati mtsinje wosefukira, umene ufikira m'khosi, kupeta mitundu ya anthu ndi chopetera cha chionongeko; ndi chapakamwa chalakwitsa, chidzakhala m'nsagwada za anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mpweya wake uli ngati mtsinje wosefukira, wa madzi ofika mʼkhosi. Iye adzasefa anthu a mitundu ina ndi sefa wosakaza; Iye akuyika zitsulo mʼkamwa mwa anthu a mitundu ina ngati akavalo, kuti ziwasocheretse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi mpweya wace uli ngati mtsinje wosefukira, umene ufikira m'khosi, kupeta mitundu ya anthu ndi copetera ca cionongeko; ndi capakamwa calakwitsa, cidzakhala m'nsagwada za anthu.