Isaiah 30:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma inu anthu a Mulungu, mudzakondwa ndi kuimba monga m'mene mumachitira usiku pa chikondwerero chopatulika. Mudzasangalala ngati anthu opita naimba toliro ku phiri la Chauta, thanthwe la Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inu mudzakhala ndi nyimbo, monga usiku, podya phwando lopatulika; ndi mtima wokondwa, monga pomuka wina ndi chitoliro, kufikira kuphiri la Yehova, kuthanthwe la Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo inu mudzayimba mokondwa monga mumachitira usiku pa chikondwerero chopatulika. Mudzasangalala ngati anthu oyimba zitoliro popita ku phiri la Yehova, thanthwe la Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Inu mudzakhala ndi nyimbo, monga usiku, podya phwando lopatulika; ndi mtima wokondwa, monga pomuka wina ndi citoliro, kufikira ku phiri la Yehova, ku thanthwe la Israyeli,