Isaiah 30:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Malo otenthera zinthu ndi okonza kale, adakonzera mfumu ya ku Asiriya. Malowo ndi ozama ndi aakulu, odzaza ndi moto ndi nkhuni. Tsono mpweya wa Chauta, wonga ngati mtsinje wa sulufure, udzakoleza motowo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Tofeti wakonzedwa kale, inde chifukwa cha mfumu wakonzedweratu; Iye wazamitsapo, nakuzapo; mulu wakewo ndi moto ndi nkhuni zambiri; mpweya wa Yehova uuyatsa ngati mtsinje wa sulufure.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Malo otenthera zinthu akonzedwa kale; anakonzera mfumu ya ku Asiriya. Dzenje la motolo ndi lozama ndi lalikulu, ndipo muli nkhuni zambiri; mpweya wa Yehova, wangati mtsinje wa sulufule, udzayatsa motowo pa nkhunizo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Tofeti wakonzedwa kale, inde cifukwa ca mfumu wakonzedweratu; Iye wazamitsapo, nakuzapo; mulu wacewo ndi moto ndi nkhuni zambiri; mpweya wa Yehova uuyatsa ngati mtsinje wasulfure.