Isaiah 30:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nawu ulosi wonena za nyama za ku chipululu chakumwera: Akazembe akuyenda m'dziko loopsa m'mene muli mikango, mphiri ndi njoka zouluka. Amasenzetsa abulu ao mphatso zamtengowapatali ndipo chuma chao amasenzetsa ngamira zao, kupita kwa mtundu wa anthu umene sungaŵathandize.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Katundu wa zilombo za kumwera. M'dziko lovuta ndi lopweteka, kumeneko kuchokera mkango waukazi, ndi wamphongo, mphiri, ndi njoka youluka yamoto, iwo anyamula chuma chao pamsana pa abulu, ndi ang'ono zolemera zao pa malinundu a ngamira, kunka kwa anthu amene sadzapindula nao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uthenga wonena za nyama za ku Negevi: Akazembe akuyenda mʼdziko lovuta ndi losautsa, mʼmene muli mikango yayimuna ndi yayikazi, mphiri ndi njoka zaululu. Iwo amasenzetsa abulu ndi ngamira chuma chawo, kupita nazo kwa mtundu wa anthu umene sungawathandize.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Katundu wa zirombo za kumwera. M'dziko lobvuta ndi lopweteka, kumeneko kucokera mkango waukazi, ndi wamphongo, mphiri, ndi njoka youluka yamoto, iwo anyamula cuma cao pamsana pa aburu, ndi ang'ono zolemera zao pa malinundu a ngamila, kunka kwa anthu amene sadzapindula nao.