Isaiah 30:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu adandiwuza kuti, “Tsopano pita, ukalembe zimenezi pa sileti iwo akuwona, ukazilembenso m'buku, kuti kutsogolo zidzakhale umboni wosatha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsopano pita, ukalembe mauwa pamaso pao pathabwa, nuwalembe m'buku, kuti akakhalebe kunthawi yam'tsogolo, mboni ya masiku onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anandiwuza kuti, “Tsopano pita, ukalembe zimenezi mʼbuku iwo akuona ndipo lidzakhala ngati umboni wosatha masiku a mʼtsogolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsopano pita, ukalembe mauwa pamaso pao pathabwa, nuwalembe m'buku, kuti akakhalebe ku nthawi yam'tsogolo, mboni ya masiku onse.