Isaiah 31:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe Chautayo ndi wanzeru ndipo angathe kuwononga. Sabweza zimene wanena, adzalimbana ndi anthu oipa ndiponso ndi anthu amene amathandiza oipawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Iyenso ndi wanzeru, nadzatengera choipa, ndipo sadzabwezanso mau ake, koma adzaukira banja la ochita zoipa, ndi amene athandiza iwo akugwira ntchito yoipa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komatu Yehovayo ndi wanzeru ndipo angathe kuwononga, ndipo sasintha chimene wanena. Adzalimbana ndi anthu ochita zoyipa, komanso ndi amene amathandiza anthu ochita zoyipa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Iyenso ali wanzeru, nadzatengera coipa, ndipo sadzabwezanso mau ace, koma adzaukira banja la ocita zoipa, ndi amene athandiza iwo akugwira nchito yoipa.