Isaiah 31:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aejipito ndi anthu chabe, si milungu ai. Akavalo ao si mizimu, koma ndi nyama chabe. Chauta akachitapo kanthu, opereka chithandizo adzaphunthwa, olandira chithandizocho adzagwa, ndipo onsewo adzathera limodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Aejipito ndiwo anthu, si Mulungu; ndi akavalo ao ali nyama, si mzimu; ndipo pamene Yehova adzatambasula dzanja lake, wothandiza adzaphunthwa, ndi wothandizidwa adzagwa, ndipo iwo onse awiri pamodzi adzalephera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aigupto ndi anthu chabe osati Mulungu; akavalo awo ndi nyama chabe osati mizimu. Yehova akangotambasula dzanja lake, amene amapereka chithandizo adzapunthwa, amene amalandira chithandizocho adzagwa; onsewo adzathera limodzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Aaigupto ndiwo anthu, si Mulungu; ndi akavalo ao ali nyama, si mzimu; ndipo pamene Yehova adzatambasula dzanja lace, wothandiza adzapunthwa, ndi wothandizidwa adzagwa, ndipo iwo onse awiri pamodzi adzalephera.