Isaiah 31:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adandiwuza kuti, “Monga momwe mkango kapena msona wa mkango umabangulira utagwira nyama, ndipo abusa sangaupirikitse, ngakhale auwopseze ndi kufuula chotani, motero palibe chimene chingaletse Chauta Wamphamvuzonse kutchinjiriza Phiri la Ziyoni ndi gomo lake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Yehova atero kwa ine, Monga mkango, ndi mwana wa mkango wobangula pa nyama yake, sudzaopa mau a khamu la abusa oitanidwa kuupirikitsa, ngakhale kudzichepetsa wokha, chifukwa cha phokoso lao; motero Yehova wa makamu adzatsikira kumenyana nkhondo kuphiri la Ziyoni, ndi kuchitunda kwake komwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zimene Yehova akunena kwa ine ndi izi: “Monga mkango kapena msona wamkango umabangula ukagwira nyama yake, ndipo suopsedwa kapena kusokonezeka ndi kufuwula kwa abusa amene akulimbana nayo, momwemonso palibe chingaletse Yehova Wamphamvuzonse kubwera kudzatchinjiriza phiri la Ziyoni ndi zitunda zake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Yehova atero kwa ine, Monga mkango, ndi mwana wa mkango wobangula pa nyama yace, sudzaopa mau a khamu la abusa oitanidwa kuupitikitsa, ngakhale kudzicepetsa wokha, cifukwa ca phokoso lao; motero Yehova wa makamu adzatsikira kumenyana nkhondo ku phiri la Ziyoni, ndi kucitunda kwace komwe.