Isaiah 31:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Aasiriya adzaonongedwa pa nkhondo, osati ndi mphamvu ya munthu. Adzaonongedwa ndi lupanga, lupanga lake osati la munthu. Adzathaŵa ku nkhondo, ndipo anyamata ao adzakhala akapolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Asiriya adzagwa ndi lupanga losati la munthu; ndi lupanga losati la anthu lidzammaliza iye; ndipo iye adzathawa lupanga, ndi anyamata ake adzalamba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Aasiriya adzaphedwa ku nkhondo ndi mphamvu osati za munthu. Lupanga, osati la munthu, lidzawawononga. Adzathawa ku nkhondo ndipo anyamata awo adzagwira ntchito yathangata.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Asuri adzagwa ndi lupanga losati la munthu; ndi lupanga losati la anthu lidzammariza iye; ndipo iye adzathawa lupanga, ndi anyamata ace adzalamba.