Isaiah 31:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu yao idzathaŵa ndi mantha, ndipo atsogoleri ake ankhondo adzabalalika mwamantha kwambiri, kotero kuti adzasiya mbendera zao zankhondo,” akutero Chauta amene moto wake uli ku Ziyoni, ndipo ching'anjo chake chili ku Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mwala wake udzachoka, chifukwa cha mantha, ndi akalonga ake adzaopa mbendera, ati Yehova, amene moto wake uli m'Ziyoni, ndi ng'anjo yake m'Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu yawo idzamwalira ndi mantha, ndipo atsogoleri awo ankhondo adzathawa ndi mantha kusiya pambuyo mbendera yawo ya nkhondo.” Akutero Yehova, amene moto wake uli mu Ziyoni, ndipo ngʼanjo yake ili mu Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mwala wace udzacoka, cifukwa ca mantha, ndi akalonga ace adzaopa mbendera, ati Yehova, amene moto wace uli m'Ziyoni, ndi ng'anjo yace m'Yerusalemu.