Isaiah 32:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nyumba yaufumu idzasiyidwa, ndipo mzinda wonse udzakhala wopanda anthu. Malinga ake ndi nsanja yomwe zidzasanduka mapanga mpaka muyaya. Abulu akuthengo adzasangalala kumeneko, ndipo ziŵeto zidzapeza busa komweko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pakuti nyumba ya mfumu idzasiyidwa; mudzi wa anthu ambiri udzakhala bwinja; chitunda ndi nsanja zidzakhala nkhwimba kunthawi zonse, pokondwera mbidzi podyera zoweta;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nyumba yaufumu idzasiyidwa, mzinda waphokoso udzakhala wopanda anthu; malinga ndi nsanja zidzasanduka chipululu mpaka muyaya. Abulu adzasangalalamo ndipo ziweto zidzapezamo msipu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pakuti nyumba ya mfumu idzasiyidwa; mudzi wa anthu ambiri udzakhala bwinja; citunda ndi nsanja zidzakhala nkhwimba ku nthawi zonse, pokondwera mbidzi podyera zoweta;