Isaiah 32:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aliyense mwa iwo adzakhala ngati pothaŵirapo mphepo ndi malo obisalirapo namondwe. Adzakhala ngati mitsinje yoyenda m'dziko louma, ndipo ngati mthunzi wa thanthwe lalikulu m'chipululu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munthu adzakhala monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m'malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m'dziko lotopetsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu aliyense adzakhala ngati pothawirapo mphepo ndi malo obisalirapo namondwe, adzakhala ngati mitsinje ya mʼchipululu, ngati mthunzi wa thanthwe lalikulu la mʼdziko lowuma.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo munthu adzakhala monga pobisalira mphepo, ndi pousira cimphepo; monga mitsinje yamadzi m'malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikuru m'dziko lotopetsa.