Isaiah 32:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu wopusa amalankhula zauchitsilu, ndipo amaganiza kuchita zoipa. Amachita zoipira Mulungu, amalankhula zonyoza Mulungu. Anjala saŵapatsa chakudya, aludzu saŵapatsa chakumwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti wopusa adzanena zopusa, ndi mtima wake udzachita mphulupulu, kuchita zoipitsa, ndi kunena za Yehova molakwira, kusowetsa konse mtima wanjala, ndi kulepheretsa chakumwa cha waludzu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti munthu opusa amayankhula zauchitsiru, amaganiza kuchita zoyipa: Iye amachita zoyipira Mulungu, ndipo amafalitsa zolakwika zokhudza Yehova; anjala sawapatsa chakudya ndipo aludzu sawapatsa madzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti wopusa adzanena zopusa, ndi mtima wace udzacita mphulupulu, kucita zoipitsa, ndi kunena za Yehova molakwira, kusowetsa konse mtima wanjala, ndi kulepheretsa cakumwa ca waludzu.