Isaiah 32:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu wachabechabe njira zake nzoipa. Amalingalira zaupandu kuti aŵachite chiwembu anthu osauka pakuŵanamizira, ngakhale pamene osaukawo ali osalakwa konse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zipangizonso za womana zili zoipa; iye apangira ziwembu zakuononga waumphawi ndi mau onama, ngakhale pamene wosowa alankhula zoona.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu woyipa njira zake ndi zoyipanso, iye kwake nʼkulingalira zinthu zoyipa. Amalingalira zakuti awononge anthu aumphawi ndi mabodza ake ngakhale kuti waumphawiyo akuyankhula zoona.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zipangizonso za womana ziri zoipa; iye apangira ziwembu zakuononga waumphawi ndi mau onama, ngakhale pamene wosowa alankhula zoona.