Isaiah 33:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsoka kwa iwe woonongawe, iwe amene sadakuwononge. Tsoka iwe wonyengawe, amene wina aliyense sadakunyenge. Iwe ukadzaleka kuwononga, adzakuwononga, ukadzaleka kunyenga, adzakunyenga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsoka kwa iwe amene usakaza, chinkana sunasakazidwa; nupangira chiwembu, chinkana sanakupangire iwe chiwembu! Utatha kusakaza, iwe udzasakazidwa; ndipo utatha kupangira chiwembu, iwo adzakupangira iwe chiwembu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsoka kwa iwe, iwe wowonongawe, amene sunawonongedwepo! Tsoka kwa iwe, iwe mthirakuwiri, iwe amene sunanyengedwepo! Iwe ukadzaleka kuwononga, udzawonongedwa, ukadzasiya umʼthirakuwiri, adzakuwononga, ndipo ukadzaleka kuchita zachinyengo adzakunyenga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsoka kwa iwe amene usakaza, cinkana sunasakazidwa; nupangira ciwembu, cinkana sanakupangira iwe ciwembu! Utatha kusakaza, iwe udzasakazidwa; ndipo utatha kupangira ciwembu, iwo adzakupangira iwe ciwembu.