Isaiah 33:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mu mzinda wa Ziyoni anthu ochimwa agwidwa ndi mantha, anthu osasamala za Mulungu akunjenjemera. Akunena kuti, “Ndani mwa ife angathe kupirira m'moto woonongawo? Ndani mwa ife angathe kukhalamo m'moto wosatha?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ochimwa a m'Ziyoni ali ndi mantha, kunthunthumira kwadzidzimutsa anthu opanda Mulungu. Ndani mwa ife adzakhala ndi moto wakunyeketsa? Ndani mwa ife adzakhala ndi zotentha zachikhalire?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mu mzinda wa Ziyoni anthu ochimwa agwidwa ndi mantha; anthu osapembedza Mulungu akunjenjemera: Iwo akunena kuti, “Ndani wa ife angathe kukhala mʼmoto wonyeketsa? Ndani wa ife angathe kukhala moto wosatha?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ocimwa a m'Ziyoni ali ndi mantha, kunthunthumira kwadzidzimutsa anthu opanda Mulungu. Ndani mwa ife adzakhala ndi moto Wakunyeketsa? ndani mwa ife adzakhala ndi zotentha zacikhalire?