Isaiah 33:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zingwe za zombo za adani athu zamasuka, sizingathe kulimbitsa mlongoti wake, ndipo matanga ake sangathe kufunyuluka. Tsono zofunkha zathu zidzakhala zochuluka kwambiri, kotero kuti pogaŵana, ndi opunduka omwe adzalandirako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zingwe zako za ngalawa zamasulidwa; sizinathe kulimbitsa patsinde pa mlongoti wake, sizinathe kufutukula matanga; pamenepo ndipo cholanda chachikulu, chofunkha chinagawanidwa; wopunduka nafumfula.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zingwe za sitima zapamadzi za adani athu zamasuka, sizikutha kulimbitsa mlongoti wake, matanga ake sakutheka kutambasuka. Ngakhale tidzagawana zofunkha zochuluka kwambiri ndipo ngakhale olumala adzatenga zofunkhazo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zingwe zako za ngalawa zamasulidwa; sizinathe kulimbitsa patsinde pa mlongoti wace, sizinathe kufutukula matanga; pamenepo ndipo colanda cacikulu, cofunkha cinagawanidwa; wopunduka nafumfula.