Isaiah 33:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dziko likulira ndipo likunka lilikutha. Nkhalango za ku Lebanoni zafota, ndipo chigwa chachonde cha Saroni chasanduka chipululu. Mitengo ya ku dera la Basani ndi ya ku phiri la Karimele ikuyoyoka masamba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Dziko lirira maliro ndi kulefuka; Lebanoni ali ndi manyazi, nafota; Saroni afanana ndi chipululu; pa Basani ndi Karimele papukutika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dziko likulira ndipo likunka likutha. Nkhalango ya Lebanoni ikuchita manyazi, yafota. Chigwa cha chonde cha Saroni chasanduka chachidalala. Masamba a mitengo ya ku Basani ndi Karimeli akuyoyoka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Dziko lilira maliro ndi kulefuka; Lebano ali ndi manyazi, nafota; Saroni afanana ndi cipululu; pa Basana ndi Karimeli papukutika.