Isaiah 34:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu anthu a mitundu yonse, bwerani pafupi kuti mumve, inu anthu onse tcherani makutu! Limvetsere dziko pamodzi ndi zonse zokhalamo, limvetsere dziko lapansi pamodzi ndi zonse zofuma m'menemo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Idzani pafupi, amitundu inu, kuti mumve; mverani anthu inu, dziko ndi zinthu zonse zotulukamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu anthu a mitundu yonse, bwerani pafupi kuti mumve: tcherani khutu, inu anthu a mitundu ina yonse: Limvetsere dziko lapansi pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo, dziko lonse pamodzi ndi zonse zochokera mʼmenemo!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Idzani pafupi, amitundu inu, kuti mumve; mverani anthu inu, dziko limve, ndi za mommo; dziko ndi zinthu zonse zoturukamo.