Isaiah 34:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'dzikomo muzidzakhala akabaŵi ndi nungu, akadzidzi ndi makwangwala. Chauta adzalisandutsanso dziko loguga ndi lopanda kanthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma vuwo ndi nungu zidzakhalamo, ndipo kadzidzi ndi khungubwi adzakhala m'menemo, ndipo Mulungu adzatambalika pamenepo chingwe choongolera cha chisokonezo, ndi chingwe cholungamitsa chilili chosatha kuchita kanthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼdzikomo mudzakhala akabawi ndi anungu; amantchichi ndi akhwangwala adzapanga zisa zawo mʼmenemo. Mulungu adzatambalitsa pa Edomu chingwe choyezera cha chisokonezo ndi chingwe chowongolera cha chiwonongeko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma bvuo ndi nungu zidzakhalamo, ndipo kadzidzi ndi khungubwi adzakhala m'menemo, ndipo Mulungu adzatambalika pamenepo cingwe coongolera ca cisokonezo, ndi cingwe colungamitsa ciriri cosatha kucita kanthu.