Isaiah 34:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akadzidzi adzamangako zisa zao, nkuikirako mazira, ndi kuswa ana ao namaŵasamala. Adembo adzasonkhana kumeneko aŵiriaŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kumeneko kadzidzi adzapanga chisa chake, naikira, naumatira, naswa mumthunzi mwake; inde kumeneko miimba idzasonkhana wonse ndi unzake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kadzidzi adzamangako chisa chake nʼkuyikirako mazira, adzaswa ana ake ndi kusamalira ana ake mu mthunzi wa mapiko ake; akamtema adzasonkhananso kumeneko, awiriawiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kumeneko njoka yotumpha idzapanga cisanja cace, niikira, niumatira, niswa mumthunzi mwace; inde kumeneko miimba idzasonkhana wonse ndi unzace.