Isaiah 34:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Funafunani ndi kuŵerenga m'buku la Chauta. Mwa zolengedwazi palibe chimene chidzasoŵa, ndipo sipadzakhala nchimodzi chomwe chopanda chinzake. Pakuti Chauta walamula kuti zitero, ndipo mzimu wake wazisonkhanitsa pamodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Funani inu m'buku la Yehova, nimuwerenge; palibe umodzi wa iye udzasowa, palibe umodzi udzasowa unzake; pakuti pakamwa pa Yehova panena, ndipo mzimu wake wasonkhanitsa iwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Funafunani mʼbuku la Yehova ndi kuwerenga: mwa zolengedwazi palibe chimene chidzasowa; sipadzakhala nʼchimodzi chomwe chopanda chinzake. Pakuti Yehova walamula kuti zitero, ndipo Mzimu wake udzawasonkhanitsa pamodzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Funani inu m'buku la Yehova, nimuwerenge; palibe umodzi wa iye udzasowa, palibe umodzi udzasowa unzace; pakuti pakamwa pa Yehova panena, ndipo mzimu wace wasonkhanitsa iwo.