Isaiah 34:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta ndiye wagaŵa dzikolo, wapatsa chilichonse chigawo chake. Dzikolo lidzakhala lao mpaka muyaya, ndipo zidzakhala m'menemo pa mibadwo yonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Iye wachita maere, chifukwa cha zilombozi, ndipo dzanja lake lazigawira dzikolo ndi chingwe, zidzakhala nalo nthawi zonse ku mibadwomibadwo, zidzakhala m'menemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova wagawa dziko lawo; wapatsa chilichonse chigawo chake. Dziko lidzakhala lawo mpaka muyaya ndipo zidzakhala mʼmenemo pa mibado yonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Iye wacita maere, cifukwa ca zirombozi, ndipo dzanja lace lazigawira dzikolo ndi cingwe, zidzakhala nalo nthawi zonse ku mibadwo mibadwo, zidzakhala m'menemo.