Isaiah 34:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakuti Chauta waŵakwiyira anthu a mitundu yonse, waŵapsera mtima magulu ao onse ankhondo, watsimikiza kuti adzaonongedwa, waŵapereka kuti aphedwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Yehova akwiyira amitundu onse, nachitira ukali khamu lao lonse; Iye wawaononga psiti, wawapereka kukaphedwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova wayipidwa ndi anthu a mitundu yonse; wapsera mtima magulu awo onse ankhondo. Iye adzawawononga kotheratu, nawapereka kuti aphedwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Yehova akwiyira amitundu onse, nacitira ukali khamu lao lonse; Iye wawaononga psiti, wawapereka kukaphedwa,