Isaiah 34:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dzuŵa, mwezi ndi nyenyezi zidzanyenyeka, ndipo mlengalenga udzakulungika monga chimachitira chikopa. Nyenyezi zonse zidzayoyoka monga amachitira masamba a mpesa kapena a mkuyu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo makamu onse a kumwamba adzasungunuka, ndi miyamba idzapindika pamodzi ngati mpukutu; makamu ao onse adzafota monga tsamba limafota pampesa ndi kugwa, ndi monga tsamba lifota pamkuyu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dzuwa, mwezi ndi nyenyezi zidzasungunuka ndipo mlengalenga mudzakulungidwa ngati chipepala; nyenyezi zonse zidzayoyoka ngati masamba ofota a mphesa, ngati masamba onyala a mtengo wa mkuyu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo makamu onse a kumwamba adzasungunuka, ndi miyamba idzapindika pamodzi ngati mpukutu; makamu ao onse adzafota monga tsamba limafota pampesa ndi kugwa, ndi monga tsamba lifota pamkuyu.